10 Musamlirire wakufa, musacite maliro ace; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.
11 Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwace mwa Yosiya atate wace, amene anaturuka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iri yonse;
12 koma kumene anamtengera iye ndende, kumeneko adzafa, ndipo sadzaonanso dziko ili.
13 Tsoka iye amene amanga nyumba yace ndi cisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi cosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzace nchito osamlipira, osampatsa mphotho yace;
14 amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikuru, nadziboolera mazenera; nabvundima chindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.
15 Kodi udzakhala mfumu, cifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadya ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? kumeneko kunamkomera.
16 Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? ati Ambuye.