2 Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israyeli, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse, kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.
3 Kapena nyumba ya Yuda idzamva coipa conse cimene nditi ndidzawacitire; kuti abwerere yense kuleka njira yace yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi cimo lao.
4 Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m'buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.
5 Ndipo Yeremiya anauza Baruki, kuti, Ndaletsedwa sindithai kulowa m'nyumba ya Yehova;
6 koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene aturuka m'midzi yao.
7 Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yace yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukuru.
8 Ndipo Baruki mwana wa Neriya anacita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri, nawerenga m'buku mau a Yehova m'nyumba ya Yehova.