8 Pamenepo, bvalani ciguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wakuopsya wa Yehova sunabwerera pa ife.
9 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzatayika, ndi mitima ya akuru; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa.
10 Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mu'dzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.
11 Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yocokera ku mapiri oti se m'cipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosaungula, yosayeretsa;
12 mphepo yolimba yocokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo.
13 Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magareta ace ngati kabvumvulu; akavalo ace athamanga kopambana mphungu, Tsoka ife! pakuti tapasuka.
14 Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kucotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako acabe agona mwako masiku angati?