27 Iphani ng'ombe zamphongo zace zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.
28 Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babulo, kuti alalikire m'Ziyoni kubwezera cilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.
29 Memezani amauta amenyane ndi Babulo, onse amene akoka uta; mummangire iye zitando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wace yense; mumbwezere iye monga mwa nchito yace; monga mwa zonse wazicita, mumcitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israyeli.
30 Cifukwa cace anyamata ace adzagwa m'miseu yace, ndi anthu ankhondo ace onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova.
31 Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.
32 Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'midzi yace, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.
33 Yehova wa makamu atero: Ana a Israyeli ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.