11 Nditani nazo nsembe zanu zocurukazo? ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde.
12 Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna cimeneci m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?
13 Musadze nazonso, nsembe zacabecabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano.
14 Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi za mapwando anu mtima wanga uzida; zindibvuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.
15 Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pocurukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.
16 Sambani, dziyeretseni; cotsani macitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kucita zoipa;
17 phunzirani kucita zabwino; funani ciweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.