5 Iwe Asuri cibonga ca mkwiyo wanga, ndodo m'dzanja lace muli ukali wanga!
6 Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala.
7 Koma iye safuna cotero, ndipo mtima wace suganizira cotero, koma mtima wace ulikufuna kusakaza, ndi kuduladula amitundu osawerengeka.
8 Popeza ati, Akalonga anga kodi sali onse mafumu?
9 Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemesi? kodi Hamati sali ngati Aripadi? kodi Samariya sali ngati Damasiko?
10 Popeza dzanja langa lapeza maufumu a mafano, mafano ao osema anapambana ndi iwo a ku Yerusalemu ndi ku Samariya;
11 monga ndacitira Samariya ndi mafano ace, momwemo kodi sindidzacitira Yerusalemu ndi mafano ace?