13 Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wacifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;
14 ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.
15 Koma udzatsitsidwa kunsi ku manda, ku malekezero a dzenje.
16 Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;
17 amene anapululutsa dziko, napasula midzi yace, amene sanamasula ndende zace, zinke kwao?
18 Mafumu onse a amitundu, onsewo agona m'ulemerero yense kunyumba kwace.
19 Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati cobvala ca ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira ku miyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.