1 Tumizani inu ana a nkhosa kwa wolamulira wa dziko kucokera ku Sela kunka kucipululu, mpaka ku phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.
2 Pakuti ana akazi a Moabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati cisa cofwancuka.
3 Citani uphungu, weruzani ciweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opitikitsidwa, osaulula woyendayenda.
4 Opitikitsidwa a Moabu akhale ndi iwe, khala iwe comphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko.
5 Ndipo mpando wacifumu udzakhazikika m'cifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'cihema ca Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa ciweruziro, nadzafulumira kucita cilungamo.