7 Tsiku limenelo munthu adzayang'ana kwa Mlengi wace, ndipo maso ace adzalemekeza Woyera wa Israyeli.
8 Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, nchito ya manja ace, ngakhale kulemekeza cimene anacipanga ndi zala zace, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.
9 Tsiku limenelo midzi yace yolimba idzakhala ngati mabwinja a m'nkhalango, ndi a pansonga pa phiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israyeli; ndipo padzakhala bwinja.
10 Cifukwa iwe waiwala Mulungu wa cipulumutso cako, sunakumbukira thanthwe la mphamvu zako; cifukwa cace iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zacilendo;
11 tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwace; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la cisoni cothetsa nzeru.
12 Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene apfuula ngati kukukuma kwa nyanja: ndi kuthamanga kwa amitundu, akuthamanga ngati kuthamangakwa madzi amphamvu!
13 Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patari, nadzapitikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga pfumbi lokwetera patsogolo pa mkunthu wa mphepo.