20 Ndipo cidzakhala cizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Aigupto; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, cifukwa ca osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.
21 Ndipo Yehova adzadziwika kwa Aigupto, ndipo Aaigupto adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kucitadi.
22 Ndipo Yehova adzakantha Aigupto kukantha ndi kuciritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawaciritsa.
23 Tsiku limenelo padzakhala khwalala locokera m'Aigupto kunka ku Asuri, ndipo M-asuri adzafika ku Aigupto, ndi M-aigupto adzafika ku Asuri, ndipo Aaigupto adzapembedzera pamodzi ndi Aasuri.
24 Tsiku limenelo Israyeli ndi Aigupto ndi Asuri atatuwa, adzakhala mdalitso pakati pa dziko lapansi;
25 pakuti Yehova wa makamu wadalitsa iwo, ndi kuti, Odalitsika Aigupto anthu anga, ndi Asuri nchito ya manja anga, ndi Israyeli colowa canga.