1 Katundu wa cipululu ca kunyanja. Monga akabvumvulu a kumwela apitirira, kufumira kucipululu ku dziko loopsya.
2 Masomphenya obvuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Media iwe; kuusa moyo kwace konse ndakutonthoza.
3 Cifukwa cace m'cuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndicita mantha sindingathe kuona.
4 Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; cizitezite cimene ndinacikhumba candisandukira kunthunthumira.