3 Cifukwa cace m'cuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndicita mantha sindingathe kuona.
4 Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; cizitezite cimene ndinacikhumba candisandukira kunthunthumira.
5 Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta cikopa.
6 Pakuti Ambuye atero kwa ine, Muka, ika mlonda anene cimene aciona;
7 ndipo pamene iye anaona khamu, amuna apakavalo awiri awiri, khamu la aburu, khamu la ngamila, iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa.
8 Ndipo iye anapfuulitsa ngati mkango, Ambuye inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthawi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse;
9 ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apaakavalo awiri awiri. Ndipo iye anayankha nati, Babulo wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yace asweka, nagwa pansi.