5 Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ace omwe, cifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, natyola cipangano ca nthawi zonse.
6 Cifukwa cace citemberero cadya dziko, ndi amene akhala m'menemo apezedwa ocimwa, cifukwa cace okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu owerengeka atsala.
7 Vinyo watsopano alira, mpesa ulefuka, mitima yonse yokondwa iusa moyo.
8 Kusangalala kwa mangaka kwalekeka, phokoso la iwo amene aserera litha, kukondwa kwa mngoli kwalekeka.
9 Iwo sadzamwa vinyo ndi kuyimba nyimbo; cakumwa caukali cidzawawa kwa iwo amene acimwa.
10 Mudzi wosokonezeka wagwetsedwa pansi; nyumba zonse zatsekedwa, kuti asalowemo munthu.
11 Muli mpfuu m'makwalala cifukwa ca vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha.