2 Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene ucita zoonadi, ulowemo.
3 Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weni weni, cifukwa ukukhulupirirani Inu.
4 Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lacikhalire.
5 Cifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa pfumbi.
6 Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphawi, ndi mapondedwe a osowa.
7 Njira ya wolungama iri njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.
8 Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi cikumbukilo canu.