9 Cifukwa cace, mwa ici coipa ca Yakobo cidzafafanizidwa, ndipo ici ndi cipatso conse cakucotsa cimo lace; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.
10 Pakuti mudzi wocingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati cipululu; mwana wa ng'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamariza nthambi zace.
11 Ponyala nthambi zace zidzatyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; cifukwa cace Iye amene anawalenga sadzawacitira cisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.
12 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wace, kucokera madzi a nyanja, kufikira ku mtsinje wa Aigupto, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israyeli.
13 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikuru lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asuri, ndi opitikitsidwa a m'dziko la Aigupto; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.