4 Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi koturuka m'pfumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kucokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong'ona kocokera m'pfumbi,
5 Koma khamu la acilendo ako lidzafanana ndi pfumbi losalala, ndi khamu la oopsya lidzakhala monga mungu wocokacoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi.
6 Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi cibvomezi, ndi mkokomo waukuru, kabvumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.
7 Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Arieli, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lace, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku.
8 Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m'kati mwace muli zi; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo, taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m'kati mwace muli gwa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni.
9 Khalani ndi kudabwa; sangalalani ndi kukhala akhungu; iwo aledzera, koma si ndi vinyo, ali dzandi dzandi; koma si ndi cakumwa caukali.
10 Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli.