1 Tsoka kwa iwe amene usakaza, cinkana sunasakazidwa; nupangira ciwembu, cinkana sanakupangira iwe ciwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira ciwembu, iwo adzakupangira iwe ciwembu.
2 Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, cipulumutso cathunso m'nthawi ya mabvuto.
3 Pa mau a phokoso mitundu ya anthu yathawa; ponyamuka iwe amitundu abalalika,
4 Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga madzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.
5 Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi ciweruzo ndi cilungamo.
6 Ndipo kudzakhala cilimbiko m'nthawi zako, cipulumutso cambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko cumacace.