13 Imvani inu amene muli kutari, cimene ndacita ndi inuamene muli pafupi, bvomerezani mphamvu zanga,
14 Ocimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto Wakunyeketsa? ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zacikhalire?
15 Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ace kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ace kusamva za mwazi, natsinzina maso ace kusayang'ana coipa;
16 iye adzakhala pamsanje; malo ace ocinjikiza adzakhala malinga amiyala; cakudya cace cidzapatsidwa kwa iye; madzi ace adzakhala cikhalire.
17 Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwace; iwo adzaona dziko lakutari.
18 Mtima wako udzaganizira zoopsya; mlembi ali kuti? ali kuti iye amene anayesa msonkho? ali kuti iye amene anawerenga nsanja?
19 Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilume lacibwibwi, limene iwe sungalimve.