15 Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ace kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ace kusamva za mwazi, natsinzina maso ace kusayang'ana coipa;
16 iye adzakhala pamsanje; malo ace ocinjikiza adzakhala malinga amiyala; cakudya cace cidzapatsidwa kwa iye; madzi ace adzakhala cikhalire.
17 Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwace; iwo adzaona dziko lakutari.
18 Mtima wako udzaganizira zoopsya; mlembi ali kuti? ali kuti iye amene anayesa msonkho? ali kuti iye amene anawerenga nsanja?
19 Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilume lacibwibwi, limene iwe sungalimve.
20 Tayang'ana pa Ziyoni, mudzi wa mapwando athu; maso ako adzaona Yerusalemu malo a phe, cihema cimene sicidzasunthidwa, ziciri zace sizidzazulidwa konse, zingwe zace sizidzadulidwa.
21 Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife m'cifumu, malo a nyanja zacitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikuru sizidzapita pamenepo.