7 Taonani, olimba mtima ao angopfuula kunja, mithenga ya mtendere ilira kowawa.
8 Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asuri watyola cipangano, wanyoza midzi, sasamalira anthu.
9 Dziko lilira maliro ndi kulefuka; Lebano ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi cipululu; pa Basana ndi Karimeli papukutika.
10 Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.
11 Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumarizani inu.
12 Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto.
13 Imvani inu amene muli kutari, cimene ndacita ndi inuamene muli pafupi, bvomerezani mphamvu zanga,