16 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
17 Cherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Sanakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.
18 Zoonadi, Yehova, mafumu a Asuri anaononga maiko onse, ndi pokhala pao.
19 Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma nchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; cifukwa cace iwo anaiononga,
20 Cifukwa cace, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwace, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.
21 Ndipo Yesaya, mwana wa Amozi, anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Popeza wandipemphera za Sanakeribu mfumu ya Asuri,
22 awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi ciphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wace pambuyo pako.