18 Zoonadi, Yehova, mafumu a Asuri anaononga maiko onse, ndi pokhala pao.
19 Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma nchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; cifukwa cace iwo anaiononga,
20 Cifukwa cace, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwace, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.
21 Ndipo Yesaya, mwana wa Amozi, anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Popeza wandipemphera za Sanakeribu mfumu ya Asuri,
22 awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi ciphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wace pambuyo pako.
23 Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? ndiye Woyera wa Israyeli.
24 Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magareta anga ine ndafika ku nsonga za mapiri, ku mbali za Lebano; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pace penipeni, ku nkhalango ya munda wace wobalitsa.