4 Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asuri mbuyace inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; cifukwa cace, kweza pemphero lako cifukwa ca otsala osiyidwa.
5 Ndipo atumiki a mfumu Hezekiya anadza kwa Yesaya.
6 Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilalatira Ine.
7 Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko la kwao.
8 Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asuri irikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inacoka ku Lakisi.
9 Ndipo anamva anthu alinkunena za Tiraka, mfumu ya Kusi, Iye waturuka kudzamenyana ndi iwe. Ndipo pamene anamva, iye anatumiza mithenga kwa Hezekiya ndi kuti,
10 Mukati kwa Hezekiya, mfumu ya Yuda, Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sadzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asuri.