6 Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzacinjiriza mudzi uno.
7 Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe cocokera kwa Yehova, kuti Yehova adzacita ici wanenaci;
8 taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.
9 Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atacira nthenda yace.
10 Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.
11 Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;
12 Pokhala panga pacotsedwa, pandisunthikira monga hema wambusa;Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba;Iye adzandidula ine poomberapo;Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.