2 Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yace ya cuma, siliva, ndi golidi, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba yonse ya zida zace, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zace; munalibe kanthu m'nyumba mwace, kapena m'dziko lace lonse, kamene Hezekiya sanawaonetsa.
3 Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo acokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo acokera ku dziko lakutari, kudza kwa ine, kunena ku Babulo.
4 Ndipo iye anati, Kodi iwo anaona ciani m'nyumba mwanu? Ndipo Hezekiya anayankha, Zonse za m'nyumba mwanga iwo anaziona; palibe kanthu ka mwa cuma canga, kamene ine sindinawaonetse.
5 Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Imvani mau a Yehova wa makamu.
6 Taona, masiku afika, kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zimene atate ako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babulo; sipadzatsala kanthu, ati Yehova.
7 Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'cinyumba cace ca mfumu ya ku Babulo.
8 Ndipo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova, amene iwe wanena, ali abwino. Iye anatinso, Pakuti padzakhala mtendere ndi zoonadi masiku anga.