1 Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu.
2 Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimupfuulire kwa iye, kuti nkhondo yace yatha, kuti kuipa kwace kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, cifukwa ca macimo ace onse.
3 Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti se khwalala la Mulungu wathu.
4 Cigwa ciri conse cidzadzazidwa, ndipo phiri liri lonse ndi citunda ciri conse zidzacepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala;
5 ndipo ulemerero wa Yehova udzabvumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena comweco,