4 Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa ciweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira cilamulo cace.
5 Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi cimene cituruka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;
6 Ine Yehova ndakuitana Iwe m'cilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;
7 kuti utsegule maso akhungu, uturutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, aturuke m'nyumba ya kaidi.
8 Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.
9 Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizichula; zisanabuke ndidzakumvetsani.
10 Yimbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ace kucokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse ziri m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.