8 Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.
9 Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizichula; zisanabuke ndidzakumvetsani.
10 Yimbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ace kucokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse ziri m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.
11 Cipululu ndi midzi yace ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala m'Sela ayimbe, akuwe kucokera pamwamba pa mapiri.
12 Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ace m'zisumbu.
13 Yehova adzaturuka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzapfuula, inde adzakuwa zolimba; adzacita zamphamvu pa adani ace.
14 Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula; ndakhala cete ndi kudzithungata ndekha; tsopano ndidzapfuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.