12 Wacipala acita zace ndi nsompho, nagwira nchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira nchito yace ndi mkono wace wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zace zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.
13 Mmisiri wa mitengo atambalitsa cingwe; nalilemba ndi colembera, nalikonza ndi ncerero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga maonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m'nyumba.
14 Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, ndi kudzisankhira yekha wina wa mitengo ya nkhalango; naoka mtengo wamlombwa, mvula niukulitsa.
15 Ndipo udzakhala kuti munthu autenthe; iye natengako, nauotha moto; inde auyatsa, naoca mkate; inde, apanga mlungu, naulambira, naupanga fano losema, naligwadira.
16 Iye atenthako mbali yina pamoto; ndi mbali yinayo adya nyama; akazinga zokazinga, nakhuta, inde, aotha moto, nati, Ha, ndakongonoka, ndauona moto.
17 Ndipo cotsalaco apanga mlungu, ngakhale fano lace losema; iye aligwadira, nalipembedza, nalipemphera nati, Ndipulumutse ine, cifukwa kuti ndinu mulungu wanga.
18 Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, cifukwa pamaso pao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwao kuti sangadziwitse.