7 Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwace, nukhala ciriri; pamalo pacepo sudzasunthika; inde, wina adzaupfuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zobvuta zace.
8 Kumbukirani ici, nimucirimike, mudzikumbutsenso, olakwa inu.
9 Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine;
10 ndilalikira za cimariziro kuyambira paciyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanacitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzacita zofuna zanga zonse;
11 ndiitana mbalame yolusa kucokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kucokera ku dziko lakutari; inde, ndanena, ndidzacionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzacicitanso.
12 Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutari ndi cilungamo;
13 ndiyandikizitsa cifupi cilungamo canga sicidzakhala patari, ndipo cipulumutso canga sicidzacedwa; ndipo ndidzaika cipulumutso m'Ziyoni, ca kwa Israyeli ulemerero wanga.