9 Cifukwa ca dzina langa ndidzacedwetsa mkwiyo wanga, ndi cifukwa ca kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakucotse.
10 Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso.
11 Cifukwa ca Ine ndekha, cifukwa ca Ine ndekha ndidzacita ici, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.
12 Mverani Ine, Yakobo ndi Israyeli, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womariza.
13 Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m'mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi.
14 Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzacita kufuna kwace pa Babulo, ndi mkono wace udzakhala pa Akasidi.
15 Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yace.