1 Mverani Ine, inu amene mutsata cilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani ikuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.
2 Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumcurukitsa.
3 Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ace onse abwinja; ndipo wasandutsa cipululu cace ngati Edene, ndi nkhwangwara yace ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.
4 Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kundicherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzacokera kwa ine, ndipo ndidzakhazikitsa ciweruziro canga cikhale kuunika kwa anthu.