12 Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
13 waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse cifukwa ca ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? uli kuti ukali wa wotsendereza?
14 Wam'nsinga wowerama adzamasulidwa posacedwa; sadzafa ndi kutsikira kudzenje, cakudya cace sicidzasowa.
15 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ace akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lace.
16 Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.
17 Galamuka, galamuka, imirira Yerusalemu amene unamwa m'dzanja la Yehova cikho ca ukali wace; iwe wamwa mbale ya cikho conjenjemeretsa ndi kucigugudiza.
18 Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana amuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera.