3 Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu colowa cao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.
4 Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzacitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi citonzo ca umasiye wako sudzacikumbukiranso.
5 Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lace; ndi Woyera wa Israyeli ndiye Mombolo wako; Iye adzachedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.
6 Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m'mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wocotsedwa, ati Mulungu wako.
7 Kamphindi kakang'ono ndakusiya iwe, koma ndi cifundo cambiri ndidzakusonkhanitsa.
8 M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa cikhalire ndidzakucitira cifundo, ati Yehova Mombolo wako.
9 Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso pa dziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.