1 Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndarama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndarama ndi opanda mtengo wace.
2 Bwanji inu mulikutayira ndarama cinthu cosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye cimene ciri cabwino, moyo wanu nubondwere ndi zonona.
3 Cherani Lhutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu cipangano cosatha, ndico zifundo zoona za Davide.
4 Taonani, ndampereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.
5 Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwa, ndi mtundu umene sunakudziwa udzakuthamangira, cifukwa ca Yehova Mulungu wako, ndi cifukwa ca Woyera wa Israyeli; pakuti Iye wakukometsa.
6 Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;
7 woipa asiye njira yace, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ace, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamcitira cifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.