2 Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakuturukira, ndi ulemerero wace udzaoneka pa iwe.
3 Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kuturuka kwake,
4 Tukula maso ako uunguze-unguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzacokera kutari, ndi ana ako akazi adzaleredwa pambali.
5 Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, cuma ca amitundu cidzafika kwa iwe.
6 Gulu la ngamila lidzakukuta, ngamila zazing'ono za Midyani ndi Efa; iwo onsewo adzacokera ku Seba adzabwera nazo golidi ndi zonunkhira; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.
7 Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebaioti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.
8 Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera ao?