1 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwakutsegulidwa kwa m'ndende;
2 ndikalalikire caka cokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;
3 ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa cobvala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, cobvala ca matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo achedwe mitengo ya cilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
4 Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso midzi yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.