5 Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wocirikiza; cifukwa cace mkono wanga wanga unanditengera cipulumutso, ndi ukali wanga unandicirikiza Ine.
6 Ndipo ndinapondereza anthu m'kukwiya kwanga, ndi kuwatswanya mu ukali wanga, ndi kutsanulira mwazi wa moyo wao.
7 Ndidzachula za cifundo cace ca Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wace waukuru kwa banja la Israyeli, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa cifundo cace, ndi monga mwa nchito zocuruka za cikondi cace.
8 Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangacite monyenga; comweco Iye anali Mpulumutsi wao.
9 M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pace anawapulumutsa; m'kukonda kwace ndi m'cisoni cace Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
10 Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa cisoni mzimu wace woyera, cifukwa cace Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.
11 Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ace, nati, Ali kuti Iye amene anawaturutsa m'nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lace? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wace woyera pakati pao,