10 Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi cigwa ca Akori cidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine.
11 Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mlungu wamwai gome, ndi kudzazira mlungu waimfa zikho za vinyo wosanganiza;
12 ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munacita coipa m'maso mwanga, ndi kusankha cimene Ine sindinakondwera naco.
13 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;
14 taonani, atumiki anga adzayimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wacisoni; ndipo mudzapfuula cifukwa ca kusweka mzimu.
15 Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale citemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzacha atumiki ace dzina lina;
16 comweco iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zobvuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.