4 amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;
5 amene ati, Ima pa wekha, usadze cifupi ndi ine, pakuti ine ndiri woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.
6 Taonani, calembedwa pamaso panga; sindidzakhala cete, koma ndidzabwezera, inde ndidzabwezera pa cifuwa cao,
7 zoipa zanu zanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandicitira mwano pazitunda; cifukwa cace Ine ndidzayesa nchito yao yakale ilowe pa cifuwa cao.
8 Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, momwemo ndidzacita cifukwa ca atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.
9 Ndipo ndidzaturutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira colowa cao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko.
10 Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi cigwa ca Akori cidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine.