1 Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israyeli, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupamnana.
2 Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efraimu. Ndipo mtima wace unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ace, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.
3 Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Turuka tsopano kukacingamira Ahazi, iwe ndi Seariyasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamariziro a mcerenje wa thamanda la pamtunda, ku khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsaru;
4 nukati kwa iye, Cenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, cifukwa ca zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, cifukwa ca mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.