14 Gubani ndi kuzungulira Babulo kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mibvi; pakuti wacimwira Yehova.
15 Mumpfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ace agwa; makoma ace agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; mumbwezere cilango; monga iye wacita mumcitire iye momwemo.
16 Muwathe ofesa ku Babulo, ndi iwo amene agwira zenga nyengo ya masika; cifukwa ca lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ace, nadzathawira yense ku dziko lace.
17 Israyeli ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampitikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asuri; ndipo pomariza Nebukadirezara uyo watyola mafupa ace.
18 Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzalanga mfumu ya ku Babulo ndi dziko lace, monga ndinalanga mfumu ya Asuri.
19 Ndipo ndidzabwezeranso Israyeli ku busa lace, ndipo adzadya pa Karimeli ndi pa Basana, moyo wace nudzakhuta pa mapiri a Efraimu ndi m'Gileadi.
20 Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israyeli zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zocimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati cotsala.