31 Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.
32 Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'midzi yace, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.
33 Yehova wa makamu atero: Ana a Israyeli ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.
34 Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lace Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumitse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babulo.
35 Lupanga liri pa Akasidi, ati Yehova, pa okhala m'Babulo, pa akuru ace, ndi pa anzeru ace.
36 Lupanga liri pa amatukutuku, ndipo adzapusa; lupanga liri pa anthu olimba ace, ndipo adzaopa.
37 Lupanga liri pa akavalo ao, ndi pa magareta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pace, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga liri pa cuma cace, ndipo cidzalandidwa.