18 Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.
19 Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,
20 koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; cifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.
21 Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! wodzala ciweruzowo! cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.
22 Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasanganizidwa ndi madzi.
23 Akuru ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera mirandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.
24 Cifukwa cace Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israyeli, Ha! ndidzatonthoza mtima wanga pocotsa ondibvuta, ndi kubwezera cilango adani anga;