1 Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu;
2 kuwapatulira osowa kuciweruziro, ndi kucotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!
3 Ndipo mudzacita ciani tsiku lakudza woyang'anira, ndi cipasuko cocokera kutari? mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? mudzasiya kuti ulemerero wanu?
4 Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.
5 Iwe Asuri cibonga ca mkwiyo wanga, ndodo m'dzanja lace muli ukali wanga!
6 Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala.