27 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wace adzacoka pa phewa lako, ndi gori lace pakhosi pako; ndipo gori lidzathedwa cifukwa ca kudzoza mafuta.
28 Wafika ku Aiati, wapitirira kunka ku Migroni; pa Mikimasi asunga akatundu ace;
29 wapita pampata; wagona pa Geba, Rama anthunthumira; Gibeya wa Sauli wathawa.
30 Pfuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! tamva, iwe Laisa! iwe Anatoti wosauka!
31 Madimena ali wothawathawa; okhala m'Gebimu asonkhanakutiathawe.
32 Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lace pa phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.
33 Taonani, Ambuye Yehova wa makamu adzasadza nthambi moopsya; ndipo zazitari msinkhu zidzadulidwa, ndipo zazitari zidzagwetsedwa.