3 Cifukwa cace mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za cipulumutso.
4 Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lace, mulalikire macitidwe ace mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lace lakwezedwa.
5 Muyimbire Yehova; pakuti wacita zaulemerero; cidziwike ici m'dziko lonse.
6 Tapfuula, takuwa iwe, wokhala m'Ziyoni, cifukwa Woyera wa Israyeli wa m'kati mwako ali wamkuru.