3 Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa cisoni cako, ndi nsautso yako, ndi nchito yako yobvuta, imene anakugwiritsa,
4 pamenepo udzayimbira mfumu ya ku Babulo nyimbo iyi yancinci, ndi kuti, Wobvuta wathadi! mudzi wagolidi wathadi!
5 Yehova watyola mkunkhu wa woipa, ndodo yacifumu ya wolamulira.
6 Wokantha anthu mwaukali kuwakantha cikanthire, wolamulira amitundu mokwiya, angosautsidwa wopanda womlanditsa.
7 Dziko lonse lapuma, liri du; iwo ayamba kuyimba nyimbo,
8 Inde, milombwa ikondwera ndi iwe, ndi mikungudza ya Lebano, ndi kunena, Cigwetsere iwe pansi, palibe wokwera kudzatidula ife.
9 Kunsi kwa manda kugwedezeka, cifukwa ca iwe, kukucingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuru akuru a dziko lapansi; kukweza kucokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.