6 Ife tinamva kunyada kwa Moabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwace, ndi kunyada kwace ndi mkwiyo wace; matukutuku ace ali acabe.
7 Cifukwa cace Moabu adzakuwa cifukwa ca Moabu, onse adzakuwa; cifukwa ca maziko a Kirihareseti mudzalira maliro, osautsidwa ndithu.
8 Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibimai; ambuye a mitundu atyolatyola mitengo yosankhika yace; iwo anafikira ngakhale ku Yazeri, nayendayenda m'cipululu; nthambi zace zinatasa, zinapitima panyanja.
9 Cifukwa cace ndidzalira ndi kulira kwa Yazeri, cifukwa ca mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleale; cifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mpfuu wankhondo wagwera.
10 Ndipo cikondwero ndi msangalalo zacotsedwa m'munda wapatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuyimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mpfuu wa masika amphesa.
11 Cifukwa cace m'mimba mwanga mulirira Moabu, ngati mngoli, ndi za m'mtima mwanga zilirira Kiriheresi.
12 Ndipo padzakhala kuti pamene Moabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika ku malo ace oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.