12 Nanga tsopano anzeru ali kuti? akuuze iwe tsopano; adziwe cimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kucitira Aigupto.
13 Akalonga a Zoani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asoceretsa Aigupto, amene ali mwala wa pangondya wa mapfuko ace.
14 Yehova wasanganiza mzimu wa kusaweruzika pakati pace; ndipo iwo asoceretsa Aigupto m'nchito zonse zace, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pace.
15 Aigupto sadzakhala ndi nchito, imene mutu pena mcira, pena nthambi ya kanjedza, pena mlulu zidzaigwira.
16 Tsiku limenelo Aigupto adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, cifukwa ca kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pace.
17 Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Aigupto, yense wakulichula adzamtembenukira mwamantha, cifukwa ca uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga pa dzikolo.
18 Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Aigupto yolankhula cinenero ca Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzachedwa, Mudzi wa cionongeko.